Bengo ndi mkazi wake, anapha nkhuku. Ili pa moto Bengo amaganiza kuti mkazi wake akachoka iye alawe ntchafu imodzi osadziwa kuti mkazi wake akuganizanso zomwezo.
Nkozo unamupola Bengo ndipo anapita ku toilet. Pamenepo mkazi wa ke anangonyamula chinthuli chimodzi n'kupita ku bafa kumakadya. Bengo atafika kuchokera ku toilet, anapeza mkazi wake palibe ndipo anatenganso ntchafu yosala ija nkupita ku bafa kuti naye akakhwasule.
Atatsegula anapeza mkazi wake akudya chintchafu. Mwa manyazi, Bengo anangoti "ndakubweretsera ina udyenso, wakuba iwe"