Tsiku lina bengo ataona tsitsi lake lakula kwambiri anaganiza zokameta koma ndalama analibe. Ali mnjira analingalira kenako anaitana mwana wina.
Bengo : mwanawe tiye tikametetse ulele
Mwana: Tiyeni !
Atafika ku babershop:
Bengo: iwe tandimete mpala
Ometa : okay boss
Atamaliza kumeta
Bengo: mwanawe Khala apa akumete.
Atasala pang'ono kumaliza kumeta mwana uja,
Bengo:ndikubwera ndimugulire tchipisi mwanayu
Ometa: koma mfulumire big
Bengo: just two minutes.
Ometa atamaliza kumeta anati: "kodi bambo ako akagula kutali tchipis eti? Mwana amvekere “ si abambo anga aja anangonditola panjira kuti tiye tikamete ulele”